![]() |
| Lawyer Sylvester Ayuba James |
Mmodzi mwa ma loya oziwika bwino Slyvester Ayuba James wadzuzula nthambi ya police pochita kafukufuku wa imfa ya Dr Victoria Bobe pagulu(public interrogation)
James wati zomwe nthambi ya police yachita ndi chibwana chamchombo lende pa nkhani za malamuro. Katswiriyu wati apolisi ali ndi ntchito imodzi yoti achite ndipo ndikubweletsa umboni ogwirika kwa ogamula mulandu osati kwa anthu pa Facebook.
Nayeso loya otchuka mdziko lino Khumbo Bonzo Soko wati ndizomvetsa chisoni kuti nthambi ya police ikuchita zitsuzo (Theatre) ndi nkhani ya siliyasi ngati ya imfa ya malemu Bobe.
Soko wati nthambi ya apolisi ikuyenera kuchita kafukufuku mosamalitsa kwambiri kuti maloya oyimira oganiziridwa asaziwiletu chomwe chilukuza mawa mukhothi. Iye wati apolisi akapusa nkhaniyi ikathera mokomera oganiziridwa mlandu "Washauti"
