"One year, six months. Tidakalirabetu Saulos... Imfa yowawa. Imfa yosamveka. Aaah.💔"
Izitu walemba ndi Mary Chilima, mayi wa masiye yemwe mwamuna wake, Saulos anali wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko.
Mary walemba pa tsamba lake la Facebook kuti pambuyo pa chaka ndi miyezi isanu ndi umodzi, sakumvetsabe pa za imfa ya mwamuna wake yomwe inakhuzanso anthu ena asanu ndi atatu pa ngozi ya ndege mu June chaka cha 2024.
Kudandawula kwa mayiyu kukudza, pambuyo pa malipoti atatu ;- awiri a akatswiri a zofufuza za ngozi za ndege a Germany komanso limodzi la kuno ku Malawi- ofufuza za ngoziyi.
Posachedwapa, nduna ya za chilungamo, Charles Mhango inati yawunikira malipotiwa ndipo zonse zaperekedwa ku ofesi ya mtsogoleri wa dziko lino, Peter Mutharika.
