![]() |
| Samuel Maonga |
Apolisi ku Ntcheu dzulo amanga a Samuel Maonga a zaka 24 powaganizira kuti anakakamiza ana awiri kuchotsa chimbudzi chawo pogwiritsa ntchito kamwa.
Mneneri wa polisi ya Ntcheu Inspector Jacob Khembo wati, a Maonga anapeza ana awiriwa omwe ndi a zaka 9 ndi 11 akuzithandiza m'munda wawo wosalimidwa ndipo anawakakamiza kuti achotse chimbudzicho pogwiritsa ntchito kamwa.
Iwo ati makolo a anawa anadabwa kuwona kuti anawa amakanika kudya chakudya kunyumba ndipo atawafunsa anaulura zomwe anawachita a Maonga.
Makolo anawatengera anawa kuchipatala Cha Biliwiri komwe anawapasa uphungu wam'malingaliro ndipo kenako anakayitula nkhaniyi kupolisi.
A Samuel Maonga omwe amachokera m'mudzi mwa mwa Maonga dera la mfumu yaikulu Njolomole, akuyembekezeka kuyankha mlandu wodyetsa ana zinthu zoyipa.
Credit : Zodiak
